20 Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza cosalungama cotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akuru,
21 koma mau awa amodzi okha, amene ndinapfuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.
22 Koma Felike anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lusiya kapitao wamkuru akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.
23 Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ace kumtumikira.
24 Koma atapita masiku ena, anadza Felike ndi Drusila mkazi wace, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za cikhulupiriro ca Kristu Yesu.
25 Ndipo m'mene anamfotokozera za cilungamo, ndi cidziletso, ndi ciweruziro cirinkudza, Felike anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.
26 Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; cifukwa cacenso anamuitana iye kawiri kawiri, nakamba naye.