1 Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:
2 Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;
3 makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; cifukwa cace ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.
4 Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa cibwana canga, amene anakhala ciyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;
5 andidziwa ine ciyambire, ngati afuna kucitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa cipembedzero cathu.
6 Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa ciyembekezo ca lonjezano limene Mulungu analicita kwa makolo athu;
7 kunkira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Cifukwa ca ciyembekezo ici, Mfumu, andinenera Ayuda.