9 Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.
10 Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.
11 Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.
12 M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe akulu, dzuwa lamsana,
13 ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kocokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa, kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.
14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'cinenedwe ca Cihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? nkukubvuta kutsalima pacothwikira.
15 Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.