18 Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Kristu, iye anakwaniritsa cotero.
19 Cifukwa cace lapani, bwererani kuti afafanizidwe macimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zocokera ku nkhope ya Ambuye;
20 ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Kristu Yesu;
21 amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulunguanalankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ace oyera ciyambire.
22 Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu ziri zonse akalankhule nanu.
23 Ndipo kudzali, kuti wamoyo ali yensesamvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.
24 Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuelindi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.