2 Ndipo munthu wina wopunduka miyendo cibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kacisi lochedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kacisi;
3 ameneyo, pakuona Petro ndi Yohane akuti alowe m'Kacisi, anapempha alandire caulere.
4 Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife.
5 Ndipo iye anabvomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu.
6 Koma Petro anati, Siliva ndi golidi ndiribe; koma cimene ndiri naco, ici ndikupatsa, M'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda,
7 Ndipo anamgwira Iye ku dzanja lace lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ace ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.
8 Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kacisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.