23 Ndipo kudzali, kuti wamoyo ali yensesamvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.
24 Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuelindi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.
25 Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.
26 Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wace, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zace.