4 Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife.
5 Ndipo iye anabvomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu.
6 Koma Petro anati, Siliva ndi golidi ndiribe; koma cimene ndiri naco, ici ndikupatsa, M'dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, yenda,
7 Ndipo anamgwira Iye ku dzanja lace lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ace ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.
8 Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kacisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.
9 Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu;
10 namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kacisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ici cidamgwera.