11 Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikuru adawadabwitsa iwo ndi matsenga ace.
12 Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwinowa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.
13 Ndipo Simoni mwini wace anakhulupiranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikilo ndi mphamvu zazikuru zirikucitika, anadabwa.
14 Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;
15 amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:
16 pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwam'dzina la Ambuye Yesu.
17 Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.