13 Ndipo Simoni mwini wace anakhulupiranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikilo ndi mphamvu zazikuru zirikucitika, anadabwa.
14 Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;
15 amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:
16 pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwam'dzina la Ambuye Yesu.
17 Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.
18 Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,
19 nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene ali yense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.