3 Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa m'nyumba m'nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.
4 Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.
5 Ndipo Filipo anatsikira ku mudzi wa ku Samarlya, nawalalikira iwo Kristu.
6 Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita.
7 Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawaturukira, yopfuula ndi mau akuru; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anaciritsidwa.
8 Ndipo panakhala cimwemwe cacikuru m'mudzimo.
9 Koma panali munthu dzina lace Simoni amene adacita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkuru;