33 M'kucepetsedwa kwace ciweruzo cace cinacotsedwa;Mbadwo wace adzaubukitsa ndani?Cifukwa wacotsedwa kudziko moyo wace.
34 Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ici za yani? za yekha, kapena za wina?
35 Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pace, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.
36 Ndipo monga anapita paniire pao, anadza ku madzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; cindiletsa ine ciani ndisabatizidwe? [
37 ]
38 Ndipo anamuuza kuti aimitse gareta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipoanambatiza iye.
39 Ndipo pamene anakwera kururuka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yace wokondwera.