2 napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.
3 Ndipo poyenda ulendo wace, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kocokera kumwamba;
4 ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?
5 Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;
6 komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.
7 Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.
8 Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.