17 Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanaziona; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva.
18 Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja.
19 Munthu ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.
20 Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;
21 ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo.
22 Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda cipatso.
23 Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.