1 Ndipo popita dzuwa la Sabata, mbanda kuca, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Mariya wa Magadala, ndi Mariya winayo, kudzaona manda.
2 Ndipo onani, panali cibvomezi cacikuru; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pace.
3 Kuonekera kwace kunali ngati mphezi, ndi cobvala cace coyeretsa ngati matalala;
4 ndipo ndi kuopsa kwace alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.
5 Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapacikidwa.
6 Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.
7 Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ace, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.