2 Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israyeli, Cikakomera inu, ndipo cikacokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'midzi yao yokhala napa podyetsa, kuti asonkhane kwa ife;
3 ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Sauli.
4 Ndipo a msonkhano onse anati kuti adzacita; pakuti cidayenera cinthuci pamaso pa anthu onse.
5 M'mwemo Davide anamemeza Aisrayeli onse kuyambira Sihori wa ku Aigupto mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriati-Yearimu.
6 Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse pamodzi naye anakwera kumka ku Baala, ndiko ku Kiriati-Yearimu wa m'Yuda, kukwera nalo kucokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.
7 Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa gareta watsopano kucokera ku nyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa garetayo,
8 Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga,