3 ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Sauli.
4 Ndipo a msonkhano onse anati kuti adzacita; pakuti cidayenera cinthuci pamaso pa anthu onse.
5 M'mwemo Davide anamemeza Aisrayeli onse kuyambira Sihori wa ku Aigupto mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriati-Yearimu.
6 Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse pamodzi naye anakwera kumka ku Baala, ndiko ku Kiriati-Yearimu wa m'Yuda, kukwera nalo kucokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.
7 Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa gareta watsopano kucokera ku nyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa garetayo,
8 Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga,
9 Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lace kulicirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka.