7 Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa gareta watsopano kucokera ku nyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa garetayo,
8 Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga,
9 Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lace kulicirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka.
10 Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, cifukwa anatambasulira likasa dzanja lace, nafa komweko pamaso pa Mulungu.
11 Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adacita cipasulo ndi Uza; motero anacha malowo Perezi Uza, mpaka lero lino.
12 Ndipo Davide anaopa Mulungu tsikulo, ndi kuti, Ndidzafika nalo bwanji likasa la Mulungu kwathu?
13 M'mwemo Davide sanafika nalo likasa kwao ku mudzi wa Davide, koma analipambutsira ku nyumba ya Obedi Edomu wa ku Giti.