37 Ndipo anasiyako ku likasa la cipangano la Yehova Asafu ndi abale ace, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;
38 ndi Obedi Edomu, ndi abale ace makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obedi Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira;
39 ndi Zadoki wansembe, ndi abale ace ansembe, ku kacisi wa Yehova, pa msanje unali ku Gibeoni;
40 kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'cilamulo ca Yehova adacilamulira Israyeli;
41 ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, ochulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti cifundo cace ncosatha;
42 ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoyimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kucipata.
43 Ndipo anacoka anthu onse, yense ku nyumba yace, nabwera Davide kudalitsa nyumba yace.