13 Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;
14 koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa cifumu wace udzakhazikika kosatha.
15 Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.
16 Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?
17 Ndipo ici ncacing'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.
18 Anenenjinso Davide kwa Inu za ulemu wocitikira mtumiki wanu? pakuti mudziwa mtumiki wanu.
19 Yehova, cifukwa ca mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwacita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikuru izi zonse.