1 Ndipo kunali, pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Yoabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yoabu anakantha Raba, naupasula.
2 Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumcotsa pamutu pace, napeza kulemera kwace talente wa golidi; panalinso miyala ya mtengo wace pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, naturutsa zankhondo za m'mudzimo zambiri ndithu.
3 Naturutsanso anthu anali m'mwemo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi zipangizo zocekera zacitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.
4 Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezeri ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Sipai wa ana a cimphona; ndipo anawagonjetsa.