1 Pamenepo Satana anaukira Israyeli, nasonkhezera Davide awerenge Israyeli.
2 Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa akuru a anthu, Kawerengeni Israyeli kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe ciwerengo cao.
3 Nati Yoabu, Yehova aonjezere pa anthu ace monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? nanga afuniranji cinthuci mbuyanga, adzaparamulitsa Israyeli bwanji?
4 Koma mau a mfumu anamlaka Yoabu. Naturuka Yoabu, nakayendayenda mwa Aisrayeli onse, nadza ku Yerusalemu.