10 Kanene kwa Davide kuti, Atero Yehova, Ndikuikira zitatu; dzisankhireko cimodzi ndikucitire ici.
11 Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko;
12 kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israyeli, Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji iye amene anandituma ine?
13 Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zace zicurukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.
14 Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israyeli; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israyeli.
15 Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka coipaci; nati kwa mthenga wakuononga, Cakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi,
16 Ndipo Davide anakweza maso ace, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lace, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akuru obvala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.