12 kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israyeli, Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji iye amene anandituma ine?
13 Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zace zicurukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.
14 Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israyeli; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israyeli.
15 Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka coipaci; nati kwa mthenga wakuononga, Cakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi,
16 Ndipo Davide anakweza maso ace, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lace, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akuru obvala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
17 Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndacimwa ndi kucita coipa ndithu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, Gnditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma Gsatsutse anthu anu ndi kuwacitira mliri.
18 Pamenepo mthenga wa Yehova anauza Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi,