1 Atakalamba tsono Davide ndi kucuruka masiku, iye analonga mwana wace Solomo akhale mfumu ya Israyeli.
2 Ndipo anasonkhanitsa akuru onse a Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi.
3 Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo ciwerengo cao kuwawerenga mmodzi mmodzi ndico amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.
4 A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira nchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi cimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,
5 ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoyimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.