5 Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.
6 Ndi Semaya mwana wa Netaneli mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleke mwana wa Abyatara, a akuru a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lace ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
7 Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, waciwiri Yedaya,
8 wacitatu Harimu, wacinai Seorimu,
9 wacisanu Malikiya, wacisanu ndi cimodzi Miyamini,
10 wacisanu ndi ciwiri Hakozi, wacisanu ndi citatu Abiya,
11 wacisanu ndi cinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya,