3 Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.
4 Komatu Yehova Mulungu wa Israyeli anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israyeli kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israyeli yense;
5 ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana amuna ambiri), anasankha Solomo mwana wanga akhale pa mpando wacifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israyeli.
6 Ndipo anati kwa ine, Solomo mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wace.
7 Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace kosatha, akalimbika kucita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.
8 Ndipo tsopano, pamaso pa Aisrayeli onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanu lanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu colowa cao kosalekeza.
9 Ndipo iwe Solomo mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna iye udzampeza, koma ukamsiya iye adzakusiya kosatha.