11 Onsewa ndiwo ana a Yedyaeli; ndiwo akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi khumi mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana awiri akuturuka kugulu kunkhondo.
12 Sufimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.
13 Ana a Nafuali: Yazieli, ndi Guni, ndi Yezeri, ndi Salumu, ana a Bila.
14 Ana a Manase ndiwo Asrieli amene mkazi wace anambala, Koma mkazi wace wamng'ono Maramu anabala Makiri atate wa Gileadi;
15 ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wace wa Hupimu ndi Supimu, dzina lace ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana waciwiri wa Manase ndiye Tselofekadi. Ndi Tselofekadi anali ndi ana akazi.
16 Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namucha dzina lace Peresi, ndi dzina la mbale wace ndiye Seresi, ndi ana ace ndiwo Ulamu, ndi Rakemu.
17 Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Gileadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.