16 Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namucha dzina lace Peresi, ndi dzina la mbale wace ndiye Seresi, ndi ana ace ndiwo Ulamu, ndi Rakemu.
17 Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Gileadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.
18 Ndi mlongo wace Hamoleketi anabala Isodi, ndi Abiezeri, ndi Mala.
19 Ndi ana a Semida ndiwo Ahiani, ndi Sekemu, ndi Liki, ndi Aniamu.
20 Ndi ana a Efraimu: Sutera, ndi Beredi mwana wace, ndi Tahati mwana wace, ndi Ekada mwana wace, ndi Tahati mwana wace,
21 ndi Zabadi mwana wace, ndi Sutela mwana wace, ndi Ezeri, ndi Eleadi, amene anthu a Gadi obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.
22 Ndipo Efraimu atate wao, anacita maliro masiku ambiri, ndi abale ace anadza kudzamtonthoza mtima.