1 Ndipo Aisrayeli onse anawerengedwa mwa cibadwidwe cao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israyeli; ndipo Yuda anatengedwa ndende kumka ku Babulo cifukwa ca kulakwa kwao.
2 Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwao mwao m'roidzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, Alevi, ndi Anetini.
3 Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efraimu ndi Manase:
4 Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omri, mwana wa Imri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.
5 Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ace.
6 Ndi a ana a Zera: Yeueli ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.