11 nalonjeza cowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukila ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wace, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pace.
12 Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pace.
13 Koma Hana ananena mu mtima; milomo yace inatukula, koma mau ace sanamveka; cifukwa cace Eli anamuyesa woledzera.
14 Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? cotsa vinyo wako.
15 Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndiri mkazi wa mtima wacisoni; sindinamwa vinyo kapena cakumwa cowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.
16 Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; cifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kucuruka kwa kudandaula kwanga ndi kubvutika kwanga.
17 Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse copempha cako unacipempha, kwa iye.