23 Ndipo Elikana mwamuna wace anati, Cita cimene cikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ace. Comweco mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wace, kufikira anamletsa kuyamwa.
24 Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye ku nyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.
25 Ndipo iwo anapha ng'ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli.
26 Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.
27 Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa copemphacanga ndinacipempha kwa iye;
28 cifukwa cace inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wace aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.