4 Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wace, ndi ana ace onse, amuna ndi akazi, gawo lao;
5 koma anapatsa Hana magawo awiri, cifukwa anakonda Hana, koma Mulungu anatseka mimba yace.
6 Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukuru, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yace.
7 Ndipo popeza munthuyo adatero caka ndi caka, popita mkaziyo ku nyumba ya Yehova, mnzaceyo amamputa; cifukwa cace iye analira misozi, nakana kudya.
8 Ndipo mwamuna wace Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? ndipo umakaniranji kudya? ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindiri wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?
9 Comweco Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wace pa mphuthu ya Kacisi wa Yehova.
10 Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;