14 Ndipo mbale wa atate wace wa Sauli ananena kwa iye ndi mnyamata wace, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna aburuwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samueli.
15 Ndipo mbale wa atate wa Sauli anati, Undiuze cimene Samueli analankhula nawe.
16 Ndipo Sauli anati kwa mbale wa atate wace, Anatiuza momveka kuti aburuwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitsa mau aja Samueli ananena zaufumuwo.
17 Ndipo Samueli anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;
18 nanena ndi ana a Israyeli, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli kuti, Ine ndinaturutsa Israyeli m'Aigupto, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aaigupto, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani;
19 koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Cifukwa cace tsono mudzionetse pamaso pa Mulungu mafuko mafuko, ndi magulu magulu.
20 Comweco Samueli anayandikizitsa mafuko onse a Israyeli, ndipo pfuko la Benjamini linasankhidwa.