3 Ndikalipo ine; citani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wace; ndinalanda ng'ombe ya yani? kapena ndinalanda buru wa yani? ndinanyenga yani? ndinasautsa yani? ndinalandira m'manja mwa yani cokometsera mlandu kutseka naco maso anga? ngati ndinatero ndidzacibwezera kwa inu.
4 Ndipo iwo anati, Simunatinyenga, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina ali yense.
5 Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wace ali mboni lero kuti simunapeza kanthu m'dzanja langa, Nati iwo, iye ali mboni.
6 Ndipo Samueli ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, naturutsanso makolo anu m'dziko la Aigupto,
7 Cifukwa cace tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova za nchito zonse zolungama za Yehova, anakucitirani inu ndi makolo anu.
8 Pamene Yakobo anafika ku Aigupto, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anaturutsa makolo anu m'Aigupto, nawakhalitsa pamalo pano,
9 Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Moabu, iwo naponyana nao.