16 Ndipo Sauli, ndi Jonatani mwana wace, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.
17 Ndipo owawanya anaturuka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofra, ku dera la Sauli;
18 gulu lina linalowa njira yonka ku Betihoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku cigwa ca Zeboimu kucipululuko.
19 Ndipo m'dziko lonse la Israyeli simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisrayeli angadzisulire malupanga kapena mikondo;
20 koma Aisrayeli onse adafotsikira kwa Afilisti, kuti awasaniire munthu yense cikhasu cace, colimira cace, nkhwangwa yace, ndi khasu lace;
21 koma analf nao matupa kukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mana ndi nkhwangwazo; ndi kusongola zothwikira.
22 Comweco kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeka mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Sauli ndi Jonatani; koma Sauli yekha ndi Jonatani mwana wace anali nazo.