33 Pamenepo anauza Sauli, kuti, Onani anthu alikucimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munacita konyenga; kunkhunizani mwala waukuru kwa ine lero.
34 Ndipo Sauli anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yace, ndi munthu yense ndi nkhosa yace, aziphe pano, ndi kuzidya, osacimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yace, usiku uja naziphera pomwepo.
35 Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.
36 Ndipo Sauli anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Citani ciri conse cikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno.
37 Ndipo Sauli anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israyeli kodi? Koma iye sanamyankha tsiku lomweli.
38 Ndipo Sauli anati, Musendere kuno, inu nonse akuru a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli coipa ici lero.
39 Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israyeli, cingakhale ciri m'mwana wanga Jonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.