7 Ndipo Sauli anakantha Aamaleki, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri; ciri pandunji pa Aigupto.
8 Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleki, naononga konse konse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.
9 Koma Sauli ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi ana a nkhosa, ndi zabwino zonse, sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konse konse.
10 Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samueli, nati,
11 Kundicititsa cisoni kuti ndinaika Sauli akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanacita malamulo anga, Ndipo Samueli anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.
12 Ndipo Samueli analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Sauli; ndipo munthu anamuuza Samueli kuti, Sauli anafika ku Karimeli, ndipo taonani, anaimika cikumbutso cace, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.
13 Ndipo Samueli anadza kwa Sauli; ndipo Sauli anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinacita lamulo la Yehova.