12 Ndipo Sauli anaopa Davide, cifukwa Yehova anali naye, koma adamcokera Sauli.
13 Cifukwa cace Sauli anamcotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wace wa anthu cikwi cimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kuturuka ndi kubwera nao.
14 Ndipo Davide anakhala wocenjera m'mayendedwe ace onse; ndipo Yehova anali naye.
15 Ndipo pamene Sauli anaona kuti analikukhala wocenjera ndithu anamuopa.
16 Koma Aisrayeli onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kuturuka ndi kulowa nao.
17 Ndipo Sauli anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkuru, dzina lace Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Sauli anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.
18 Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine ndine yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga liri lotani m'Israyeli, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?