20 Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli anakonda Davide; ndipo pakumva Sauli, anakondwera nako.
21 Nati Sauli, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Cifukwa cace Sauli ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kaciwiri.
22 Ndipo Sauli analamulira anyamata ace, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ace onse akukondani; cifukwa cace tsono, khalani mkamwini wa mfumu.
23 Ndipo anyamata a Sauli analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muciyesera cinthu copepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndiri munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.
24 Ndipo anyamata a Sauli anamuuza, kuti, Anatero Davide.
25 Nati Sauli, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna colowolera cina, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere cilango adani a mfumu. Koma Sauli anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.
26 Ndipo pamene anyamata ace anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu.