6 Ndipo Sauli anamvera mau a Jonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye.
7 Pamenepo Jonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Jonatani anafika naye Davide kwa Sauli, iye nakhalanso pamaso pace monga kale.
8 Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anaturuka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe akuru, ndipo iwo anamthawa iye.
9 Ndipo mzimu woipa wocokera kwa Yehova unali pa Sauli, pakukhala iye m'nyumba mwace, ndi mkondo wace m'dzanja lace; ndipo Davide anayimba ndi dzanja lace.
10 Ndipo Sauli anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kucoka pamaso pa Sauli; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.
11 Ndipo Sauli anatumiza mithenga ku nyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.
12 Comweco Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.