2 Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira nchito, ninena nane, Asadziwe munthu ali yense kanthu za nchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.
3 Cifukwa cace tsono muli ndi ciani? mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena ciri conse muli naco.
4 Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndiribe mkate wacabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.
5 Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; cicokere ine, zotengera za anayamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wacabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?
6 Comweco wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adaucotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anacotsa winawo.
7 Tsono munthu wina wa anyamata a Sauli anali komweko, tsiku lija, anacedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lace ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Sauli.
8 Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? cifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mrandu wa mfumu ukuti ndifulumire.