1 Ndipo kunali, pakubwerera Sauli potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku cipululu ca Engedi.
2 Tsono Sauli anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisrayeli onse, namuka kukafuna Davide ndi anthu ace m'matanthwe a zinkhoma.
3 Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Sauli analowa kuti akapfunde mapazi ace. Ndipo Davide ndi anyamata ace analikukhala m'kati mwa phangamo,
4 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamcitira iye cokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli mobisika.
5 Ndipo kunali m'tsogolo mwace kuti a mtima wa Davide unamtsutsa cifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli.
6 Nati kwa anyamata ace, Mulungu andiletse kucitira ici mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
7 Comweco Davide analetsa anyamata ace ndi mau awa, osawaloleza kuukira Sauli. Ndipo Sauli ananyamuka, naturuka m'phangamo, namuka njira yace.