1 Ndipo Samueli anamwalira; ndi Aisrayeli onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ace, namuika m'nyumba yace ku Rama. Davide nanyamuka, natsikira ku cipululu ca Parana.
2 Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wace anali ku Karimeli; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi cikwi cimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zace ku Karimeli.
3 Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wace ndiye Abigayeli; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa macitidwe ace; ndipo iye anali wa banja la Kalebi.
4 Ndipo Davide anamva kucipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zace.