25 Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; cifukwa monga dzina lace momwemo iye; dzina lace ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaona anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza.
26 Cifukwa cace tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera cilango ndi dzanja la inu nokha, cifukwa cace adani anu, ndi iwo akufuna kucitira mbuye wanga coipa, akhale ngati Nabala.
27 Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.
28 Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka coipa masiku anu onse.
29 Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga coturuka m'coponyera mwala.
30 Ndipo kudzali, pamene Yehova anacitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israyeli;
31 mudzakhala opanda cakudodoma naco, kapena cakusauka naco mtima wa mbuye wanga, cakuti munakhetsa mwazi wopanda cifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera cilango; ndipo Yehova akadzacitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukile mdzakazi wanu.