2 Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.
3 Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ace, munthu yense ndi a pabanja pace, inde Davide ndi akazi ace awiri, Ahinoamu wa ku Jezreeli, ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wa Nabala.
4 Ndipo anauza Sauli kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunanso.
5 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumiraga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wacifumu pamodzi ndi inu?
6 Ndipo Akisi anampatsa Zikilaga tsiku lomweli; cifukwa cace Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.
7 Ndipo kuwerenga kwace kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko caka cimodzi ndi miyezi inai.
8 Ndipo Davide ndi anthu ace anakwera, nathira nkhondo yobvumbulukira pa Agesuri, ndi Agirezi, ndi Aamaleki; pakuti awa ndiwo anthu akale a m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Aigupto.