1 Ndipo mwanayo Samueli anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzi kamodzi; masomphenya sanaoneka-oneka.
2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwace (maso ace anayamba cizirezire osatha kupenya bwino);
3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samueli nagona m'Kacisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.
4 Pamenepo Yehova anaitana Samueli; ndipo iye anayankha kuti, Ndiri pano.
5 Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitana, kagone. Napita iye, nagona,
6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samueli. Ndipo Samueli anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.
7 Koma Samueli sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.