4 Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.
5 Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinoamu wa ku Jezreeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.
6 Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi cisoni, yense cifukwa ca ana ace amuna ndi akazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wace.
7 Ndipo Davide ananena ndi Abyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.
8 Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Lonriola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.
9 Comweco Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.
10 Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, cifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.