7 Ndipo Davide ananena ndi Abyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.
8 Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Lonriola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.
9 Comweco Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.
10 Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, cifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.
11 Ndipo ena anapeza M-aigupto kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa cakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;
12 nampatsanso cigamphu ca ncinci ya nkhuyu ndi ncinci ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wace unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya cakudya, osamwa madzi.
13 Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? ufumira kuti? Nati iye, Ndiri mnyamata wa ku Aigupto, kapolo wa M-amaleki; mbuye wanga anandisiya, cifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.