1 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisrayeli; Aisrayeli nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Giliboa.
2 Ndipo Afilisti anapitikitsa, osawaleka Sauli ndi ana ace; ndipo Afilisti anapha Jonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisua, ana a Sauli.
3 Ndipo nkhondoyo inamkulira Sauli kwambiri, oponya mibvi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukuru cifukwa ca oponya mibviyo.
4 Tsono Sauli ananena ndi wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka, Koma woo nyamula zida zace anakana; cifukwa anaopa ndithu. Cifukwa cace Sauli anatenga lupanga lace naligwera.
5 Ndipo pakuona kuti Sauli anafa, wonyamula zida zace yemwe, anagwera lupanga lace, nafera limodzi ndi iye.
6 Comweco adamwalira pamodzi Sauli ndi ana ace atatu, ndi wonyamula zida zace, ndi anthu ace onse, tsiku lomwe lija.