10 Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisrayeli; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wace; ndipo kunali kuwapha kwakukuru; popeza anafako Aisrayeli zikwi makumi atatu a oyenda pansi.
11 Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinehasi, anaphedwa.
12 Ndipo munthu wa pfuko la Benjamini anathamanga kucokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace.
13 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wace unanthunthumira cifukwa ca likasa la Mulungu, Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.
14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.
15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ace anangokhala tong'o osapenya,
16 Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndacokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, a Nkhondoyo idatani, mwana wanga?